Mighty Tigers yapata chipambano choyamba chiyambire league

Advertisement

Timu ya WakaWaka Mighty Tigers yapata ma point ake onse atatu oyamba itaswa PremierBet Dedza Dynamos 2-0 mu masewelo otola ma point mu 2025 TNM Super League omwe anachitikira pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.

Ngakhale Dedza Dynamos inasintha malo anayi a timu yomwe inayamba masewelo a sabata yatha ndi Mzuzu City Hammers, Martin Nsewa ndi yemwe anayamba kuswabe Dedza kudzera pa penate pomwe Yasin Chida anakalawira m’malo a ngozi pa mphindi ya chi 14, (1-0)

Pa mphindi ya chi 74 chigawo chachiwiri Shukulani Afiki anapeleka mpira wangozi omwe unakapeza Precious Chiudza ndi kuwononga alendo a ku Dedza (2-0) zomwe zasuntha Tigers kufika pa nambala 10 tsopano ndi ma point ake oyamba atatu m’masewelonso atatu.

Leo Mpulula mphunzitsi wa Mighty Tigers wati lero anyamata ake awonetsako kusewera bwino kwambiri ndipo amapita kutsogolo mwa mkokomo kulekana ndi masewelo oyamba.

Andrew Bunya mphunzitsi wa Dedza Dynamos wati anawona kuti masewela a lero akhala otentha, koma masamu omwe anachita ogonjetsera Kau-Kau boys anakanika.

Iye wati anyamata ake anakanika kukhala ndi chindunji pa mpira, ndipo wati anayesetsa kupeza mipata koma sizinasinthe kubweletsa chigoli.

Dedza yagonja kachiwiri tsopano kutaya ma point asanu ndi imodzi itaswedwanso ndi Mzuzu City Hammers 1-0 koma anakwanitsa kupambana masewelo oyamba 4-1 ndi timu ya Creck Sporting.

Advertisement

Leave a CommentCancel reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.