Yembekezerani kutentha kolapitsa, pewani bibida – DCCMS

Advertisement
Hot weather

Nthambi yoona za nyengo m’dziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati nyengo yotentha ipitilira m’dziko muno ndipo aMalawi adzimwa madzi ambiri koma chakumwa chaukali achiiwale kaye.

Nthambiyi yati lero mmawa uno mm’adera ambiri kukhala nyengo yopanda mvula komanso yofunda.

“Agulu tikulangizeni bwanji kuti muyime kaye kumwa zaukali zija koma mulimbikire kumwa madzi,” yatero Nthambiyi.

DCCMS yatinso kutentha monyanyira komanso modetsa nkhawa kupitilira m’madera am’chigawo chakum’mwera.

Ntambiyi yati Lolemba sabata lino kutentha modetsa nkhawa kupitilira m’madera am’chigawo chakumwera komabe mvula ya mabingu yapatali patali ikuyembekezereka m’madera am’zigawo za kumpoto ndi pakati.

Advertisement