Bambo amangidwa kamba koba Mbuzi

Advertisement
Rumphi

Apolisi ku Rumphi amanga James Phiri wa zaka 38 yemwe akumuganizira kuti anaba mbuzi zinayi ku Luwagha.

Phiri, wa m’mudzi mwa Pinga kwa Machinga, adamangidwa pa 25 October 2024, ku Kawembe.

Iye akuyemberezeka kukaonekera kubwalo lamilandu lolemba kukayankha mlandu wakuba.

Pakali pano eniake azifuyozo azizindikira koma zikhalabe m’manja mwa apolisi pomwe akaonetse ku bwalo la milandu ngati umboni.

Advertisement