Adindo atsindika za kufunika koti pakhale lamulo lopeleka mwayi woti amayi azichotsa mimba mwandondomeko ponena kuti zingathandize kupulumutsa miyoyo yambiri yomwe ati ikutayika pano.
Izi zikubwera pomwe pa 28 September dziko lonse la pansi limakumbukira tsiku lochotsa mimba mwadongosolo, ndipo kuno ku Malawi mwambowu unachitikira m’boma la Kasungu posachedwapa.
Poyankhula pa mwambowu, phungu wa nyumba ya malamulo kunzambwe kwa boma la Chiradzulu, Matthews Ngwale, wabwerezanso kunena kuti nkofunika kuti dziko lino livomeleze lamulo lochotsa mimba mwadongosolo.
A Ngwale omweso ndi wapampando wa komiti yapadera yowona za umoyo ya kunyumba ya malamulo, ati izi zingathandize kuthana ndi chiwerengero chokwera cha akazi omwe akumafa kaamba kochotsa mimba mozemba komaso mosatsata dongosolo.
Malingana ndi bungwe la Ipas Africa Southern Region, m’chaka cha 2023 amayi oposa 35,000 adachotsa mimba mosatsata ndondomeko m’dziko muno, kuyika miyoyo yawo pa chiswe.
Money is the route of all evil