Akweni aonetsa chidwi chopikisana nawo paudindo wa mtsogoleri wa UTM

Advertisement
UTM

Pamene chisankho chosankha mtsogoleri wa dziko lino chatsala pang’ono kuchitika mdziko muno, ku chipani cha UTM nako kwayaka moto kaamba koti a Patricia Kaliati omwenso amadziwikanso ndi dzina loti Akweni, aonetsa chidwi chopikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa chipani chi.

A Kaliati omwe ndi mlembi wamkuku wa UTM, ati iwo akhala ochilimika ku chipanichi komanso chimwalilireni a Saulos Chilima pa 10 June chaka chino, iwo anaima njii kuchipani chi.

Kudzera pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, a Kaliati ati iwo ndi nkhala kale pa ndale ndipo akhala akusankhidwa kukhala Nduna ma boma onse omwe alamulira dziko la Malawi kuyambila 1994.

Akweni ati iwo ndi mnzimai ochilimika yemwe akudziwa bwino ngodya zachipani cha UTM komanso ali ndi maphunziro a PhD.

Ku msonkhano waukulu wa chipanichi omwe uchitike pa 17 November 2024, Akweni akapikisana pa pampandowu ndi a Matthews Mtumbuka, Dalitso Kabambe ndi ena.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.