Sitima ya MV Chambo ikuyambiranso maulendo ake pa Nyanja ya Malawi 

Advertisement
Likoma

Anthu okhala pa zilumba za Likoma ndi Chizumulu pakali pano ali ndi mwayi oyenda mosavuta kuchokera pa zilumbazo kufika ku Nkhata-Bay ndi madera ena pomwe Unduna wa za Mtengatenga ndi zomangamanga wati Sitima ya MV Chambo yomwe inalembetsedwa mukaundula wa Sitima ku dziko la Mozambiki iyambilenso kuyenda pa nyanja ya Malawi.

M’neneri mu undunawu Watson Maingo wati sitimayi iyamba ma ulendo ake pa 26 Sepitembala chaka chomwe chino zomwe zichepetse mavuto amayendedwe pa nyanja. 

Maingo watiso MV Chambo imathandiza anthu kuyenda panyanjayi koma idayima muchaka cha 2019 chifukwa cha mliri wa Covid 19 pomwe malire a dzikoli adatsekedwa.

Wapampando wa komiti yachitukuko m’dera la kumpoto kwa Likoma, Frank Mkali wati kubwera kwa MV Chambo kudzetsa mpumulo kwa anthu a pazilumbazi kuphatikizapo azintchito za boma.

“N’zomvetsa chisoni kuti anthu ena akulephera kuyenda bwino chifukwa anavulala polimbirana kukwera sitimayi chifukwa cha kuchulukana kwa katundu ndipo ena akhala akutaya katundu wawo,” adatero Mkali. 

Iye adaonjeza kuti anthu ena akhala akukana ntchito ku Likoma chifukwa cha mavuto omwe amakumana nawo pamadzi, zomwe ati zasokoneza anthu ogwira ntchito pachilumbachi.

Posachedwapa pakhala chipwirikiti cha mabungwe osiyanasiyana opempha boma kuti lilowererepo powonjezera zombo zina pa Nyanja ya Malawi kuti zichepetse mavuto a mayendedwe a pa madzi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.