Pomwe njala yafika posautsa m’boma la Machinga, Mfumu Yayikulu Nchinguza ya m’bomali yanena kuti pa tsiku ikulandila madando osachepera asanu ndi awiri okhudza abambo omwe akuthawa mabanja awo kuthawira mdziko la Mozambique, chifukwa cha njala yomwe yavuta m’derali.
Malingana ndi Mfumuyi, abambowa sakumabwelera pa kutha kwa nthawi, akapita kukasaka maganyu m’dziko la Mozambique, lomwe lachita malire ndi dera lake zomwe yati zikukolezera mavuto kwa ana komanso amayi.
“Mu dera langa anthu amadalira kwambiri mpunga koma zaka ziwiri zapitazi anthu sanakolole kutsatira ng’amba komanso namondwe wa Freddy yemwe anakokolola mbewu zawo ndipo izi zapangitsa kuti chiwerengelo cha anthu omwe akusowa chakudya chikwele mu dera langali,” iwo anatero.
Mfumuyi yapempha mabungwe komanso boma kuchitapo kanthu msanga pothandiza anthuwo.
“Lero lino, ndalandira kale uthenga kuti ana ena awiri omwe ndi a zaka za pakati pa 5 ndi 6 akomoka ndi njala, anawa ndiochokera madera la mfumu Kasongo komanso Mkawa, zomwe zikuonetseratu kukula kwa vuto la njala kwathu kuno,” atero a Nchinguza.
Posachedwapa Phungu wa dera la Machinga Likwenu a Bright Msaka anadandaula ku Nyumba ya Malamulo kuti anthu ena m’boma la Machinga akudya chitedze pomwe njala yafika posauzana.
A Msaka anati anthuwa akumanyika chitedzechi m’madzi kenako nkuchiswa ndikutenga nthangala zake nkuphika ngati kalongonda.
Mkulu owina za ngozi zogwa mwadzidzidzi m’bomali a Sheperd Jere analonjeza kuti pompano ayamba kugawa chakudya pomwe afikire madera onse omwe akhudzidwa ndi njala.