Paul Kagame akuganiza zokhazikitsa msonkho ku mipingo

Advertisement
Kagame

Mtsogoleri wa dziko la Rwanda, Paul Kagame, wati akuganiza zokhazikitsa msonkho pa zopereka za ku mipingo pofuna kuthana ndi vuto la abusa a Evangelical omwe akutenga nawo mbali yolanda ndikudyera anzawo masuku pa mutu.

M’mawu ake oyamba atasankhidwanso posachedwapa, Kagame adadzudzula mwa mphamvu atsogoleri azipembedzo omwe amagwiritsa ntchito maudindo awo molakwika pokakamiza anthu mowanamiza kuti awatengere ndalama.

“Anthu opanda khalidwewa amene amagwiritsa ntchito zipembedzo ndi mipingo mwachinyengo pobera anthu ndalama zawo ndi zinthu zina atipangitsa kubweretsa msonkho, choncho atchalitchi azizalipira msonkho pa ndalama zomwe amapeza kwa anthu,” adatero.

Akuluakulu aku Rwanda adalengeza sabata latha kuti atseka mipingo pafupifupi 8,000 yomwe ikugwira ntchito popanda chilolezo ndipo inalephera kumanga nyumba zopempheleramo zolingana ndi ndondomeko ya dziko.

Kagame ananenanso kuti cholinga chake ndi kulimbana ndi atsogoleri amipingo osavomerezeka ndi malo awo opemphelera.

“Ngati chowonadi chikanenedwe, mipingo yomwe ikukakamirayi yangotsala pang’ono kufinya ngakhale kakhobiri kotsala ka anthu osauka a ku Rwanda, ndipo azitsogeleriwa amazikundikira chuma okha,” adaonjezera motero.

Chiwerengelo cha mipingo ya Chipentekoste ku Rwanda chawonjezeka posachedwapa. Ambiri a iwo atengera chiphunzitso cha uthenga wabwino wotukuka, chomwe chakopa “olambira osauka” ambiri. Vuto la kuwongolera olalikira siliri ku Rwanda kokha.

Uganda idalengeza sabata zapitazo kuti ikukonzekera kutulutsa chikalata choyera chokhudza kupembedza kutsatira malipoti oti atsogoleri azipembedzo amalanda ndalama. Ku Kenya, makhoti amilandu pakali pano akulimbana ndi mlandu wa Paul Mackenzie ndi otsatira ake, omwe akuimbidwa mlandu wosokoneza olambira kuti achite nawo kusala kudya koopsa. 

Advertisement