Bodza! MANEB yatsutsa zoti mayeso a MSCE alembedwaso

Advertisement
Malawi exams

Bungwe lolembetsa mayeso la Malawi National Examination Board (MANEB) lati mphekesera yoti mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) a chaka chino alembedwaso ndi bodza la nkunkhuniza.

Izi zikubwera pomwe anthu m’masamba anchezo akhala akugawana kalata ina yomwe ikusonyeza kuti bungweli layimitsa mayeso a MSCE omwe alembedwa posachedwapa ponena kuti panali mavuto ochuluka kwambiri. 

Kalatayi yomwe pali dzina la mkulu wa MANEB, Dorothy Nampota yatchula mavuto monga kusowa kwa pepala la Map Reading pa mayeso a phunziro la Geography ngati zina mwa zifukwa zomwe likufunira kuti mayesowa alembedweso.

Koma poyankhapo za nkhaniyi, bungwe la MANEB kudzera pa tsamba lake la fesibuku lati nkhaniyi ndi bodza ndipo lati lilibe chikozero cholembetsaso mayeso aliwose.

“Bungwe la Malawi National Examinations Board likutsutsa mphekesera zomwe zakhala zikufalitsidwa kudzera pa masamba anchezo zokhuza kuchotsedwa kwa mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) a 2024,” latsutsa bungwe la MANEB.

Advertisement