Olo wina afune, asafune MCP ilowanso m’boma – atero aChakwera

Advertisement
Lazarus Chakwera

Kaya ena akumalotabe nkumaganiza kuti adzachotsa chipani cha Malawi Congress m’boma, izi ayiwale kamba koti aChakwera akuti chipani chi chilowanso m’boma chaka cha m’mawa.

A Chakwera amayankhula izi ku msonkhano waukukulu wa chipanichi ku Bingu International Convention Centre (BICC)-Lilongwe komwe amatseka msonkhano waukuluwu wa chipanichi.

Mtsogoleri wa dziko linoyu anati mamembala achipanichi akuyenera kuchilimika pogwira ntchito ndi cholinga choti aMalawi adzawavoterenso muchisankho cha mu 2025.

“Olo wina afune, kaya asafune chipani cha Malawi Congress chilowanso m’boma chaka cha m’mawa ndipo MCP siikutuluka m’boma,” anatero aChakwera.

Iwo anayamikila komiti yomwe imayendetsa msonkhano waukulu wa chipani chi motsogozedwa ndi a Kezzie Msukwa ponena kuti komitiyi yagwira ntchito yotamandika.

A Chakwera ayamikilanso ma membala ndi masapota achipani chi amene ali ndi ma bizinezi osiyanasiyana popereka ndalama zomwe zayendetsa msokhano wu.

“Analipo ena m’mbuyomu amatenga ndalama zaboma kumapangira zachipan, koma Malawi Congress siipanga nawo zimenezo. Ine ndikuona kuti kutenga misonkho ya aMalawi nkumakapangira zinthu zachipani ndikolakwika. Ife a Malawi Congress tikutenga misonkho ya aMalawi kumakamangira miseu, zipatala ndi zina zambiri,” anaonjezera aChakwera.

Iwo anapempha anthu omwe asankhidwa m’maudindo osiyanasiyanawa kuti achotse mtima odzikonda, kudzikundikila ndi makhalidwe ena omwe sakuyenera kukhala mchipani.

Polankhula pa chiyambi cha msokhanowu lero, a Kezzie Msukwa omwe amatsogolera komiti ya msokhano waukuluwu anati chipanichi m’bandakucha wa lero chataya delegeti mmodzi omwe ndi a Councillor Robert Jacob Ndhlovu.

Msonkhanuwu unatha chakumadzulo ndipo chipanichi chati mipando ina monga wachiwiri kwa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi akasankhidwa ndi a National Executive Committee (NEC). Mpando umene waonjezerekanso mchipanichi ndi wa a Moses Kunkuyu omwe asankhidwa kukhala oyang’anira zokopa anthu m’chipani chi.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.