Chipani cha MCP chayimitsa mlandu wake omwe kukhothi

Advertisement
MCP

Chipani cha Malawi Congress (MCP) chayimitsa mulandu wake omwe ku bwalo lalikulu patangopita maola ochepa chabe pomwe bwalori linaimitsa msonkhano waukulu wa chipanichi kamba ka madando omwe chipanichi chinakatula kubwalori.

Woyimila pa mlandu chipami Wapona Kita watsimikiza zakuthetsedwa kwa mulanduwu.

A Kita awuza nyumba zowulutsa mawu zosiyanasiyana kuti achita izi atalangizidwa ndi chipanichi kuti akachotse mulanduwu kamba kakuti kupanda kutero, ndalama zankhaninkhani zipita ngati msonkhano waukuluwo uyimitsidwebe.

“Ndauzidwa ndi anthu womwe ndikuwayimira pa mulanduwu kuti lingaliro lopitilira ndi apilo lachotsedwa kutanthauza kuti zomwe Khoti Lalikulu lidanena zilibe ntchito. Izi zikutanthauza kuti msonkhano wa chipanichi uchitika mawa,” iwo anatero.

Pakadali pano, nthumwi zomwe zasonkhan ku BICC zachipanichi zayamba kulembetsa maina kuti zidzathe kusankha adindo atsopano pa mipando yosiyanasiyana mchipanichi.

Mkumanowu uyamba Lachinayi mpaka Loweruka ndipo a Lazarus Chakwera akuyembekezeka kukasankhidwanso ngati mtsogoleri wa chipanichi yemwe adzaimile pa zisankho zapatatu chaka cha mawa.

Akatswiri pa nkhani za ndale ati zomwe achita akuluakulu achipanichi kuletsa ma membala ena kupikisana nawo zikuonetsera poyera kuti chipani cha MCP chilibe ulamulo wa demokilase.

Mumbuyomu chimapanichi chinalemba kalata yodzuzula chipani cha Democratic Progressive (DPP) kuti kuletsa anthu kupikisana nawo pa ma undindo mchipanichi ndi kusowa kwa demokalase.

Advertisement