Ophunzira a MUBAS akusonkhetsa thandizo la ophunzira mzawo emwe akufunikira thandizo 

Advertisement
Mubas students

Awa mukuwaona pa chinthunzipa ndi ophunzira apa sukulu ya ukachenjede ya Malawi University of Business and Applied Science (MUBAS) mu nzinda wa Blantyre ndipo iwowa akonza mwambo otolera thandizo loti lithandizire ophunzira nzawo amene akudwala nthenda ya Aplastic anaemia.

Odwalayu dzina lake ndi Fortune Milanzi, amene ali m’chaka chachiwiri pa sukuluyi ndipo akuyenera kukachitidwa opeleshoni kunja kwa dziko lino.

Malingana ndi mtsogoleri wa bungwe loimira ophunzira ku MUBAS, Gershon Nyirenda, Milanzi wakhala akudwala nthendayi kuyambira chaka chatha ndipo ndalama zokwana K30 million ndi zomwe zikufunika kuti akamuchite opeleshoni yotchedwa “bone marrow transplant” mchingerezi.

Nyirenda wati mwambo osonkhetsa thandizoli wayambira pa bwalo la masewero la Kamuzu, ndipo adutsa mtauni ya Blantyre kenako pa sukuluyi kudzera munsewu wa Masauko Chipembere Highway.

Amene akufuna kuthandiza ayimbe pa manambala awa: +256884598754/+265996622390.

Advertisement