Fomo yaluza womwetamweta

Advertisement
TNM Super League

Fomo yaluza womwetamweta pamene yalepherana ndi anyamata a Mighty Tigers.

Fomo inapeza chigoli choyamba pa mphindi khumi ndi imodzi kudzera mwa osewera Hassan Hussein.

Pamene zimakwana mphindi makumi awiri ndi ziwiri (22) naye osewera wa timuyi Hassan Luwemba anagoletsanso chigoli cha nambala 2 zomwe zinapangitsa timu ya Fomo kutsogola ndi zigoli ziwiri kwa duu.

Mphindi makumi anayi ndi zisanu (45) zitakwana oyimimbira anakoka wezulo kusonyeza kuti chigawo choyamba chatha.

Zinthu zinayamba kutembenuka mchigawo chachiwiri pamene anyamata a Mighty Tigers anabwera ndi mphamvu kuposa mkango ndipo pamphindi 53 Daniel Manda wa Tigers anagoletsa zomwe zinapangitsa kuti timuyi izitsalira ndi chigoli chimodzi.

Naye Precious Chipungu osewera wa Tigers anagoletsanso chigoli cha nambala 2 pamphindi zokwana 58, zomwe zinapangitsa kuti Fomo ndi Tigers afanane mphamvu ndi zigoli ziwili ziwiri.

Mphindi zoposa 90 zitakwana oyimbira masewerowa anakoka wezulo kusonyeza kuti masewero atha Fomo yalepherana ndi Mighty Tigers.

Advertisement