Lekani kuononga misonkho pomayenda m’misika, tsitsani mitengo ya zinthu – wadzudzura Mneneri David Mbewe

Advertisement
Prophet Mbewe Malawi

Mtsogoleri wa chipani cha Liberation for Economic Freedom (LEF) M’neneri David Mbewe, wauza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi kuti asiye kuyendera misika ponena kuti akuononga misonkho yomwe itha kugwira ntchito zina zotukura dziko lino.

Mbewe, yemweso ndi mtsogoleri wa mpingo wa Living Word Evangelistic Church (LIWEC), wayankhula izi kudzera pa tsamba lake lina la fesibuku pomwe wayika chithuzi chomwe walembapo zodandaula pa kukwera mitengo kwa zinthu.

M’chithuzicho a Mbewe ati kutsitsa mitengo yazinthu ndi kubwezeletsa Kwacha mchimake mkofunika kwambiri kuposa kupereka ngongore kwa anthu owelengeka ngati momwe a Usi alonjezera anthu m’madera angapo posachedwapa.

Iwo ati, “Mayankho amabvuto onse omwe dziko la Malawi likukumana nalo ali ku capital hill pa tabulo yanu. Lekani kuononga misonkho ya a Malawi kumayenda mmisika, mmalo mwake tsitsani mitengo yazinthu kuti aliyense apindule.”

Mneneriyu wawonjezera kuti palibe dziko lomwe lingakhalebe losauka ngati atsogoleri ake akudziwa chomwe akuchita, ndipo wati ndikofunika kusintha zinthu.

Izi zikubwera pomwe posachedwapa a Usi ayendera misika ingapo munzinda wa Blantyre komwe mwa zina awuza anthu ochita malonda osiyanasiyana kuti alembane mayina ponena kuti boma tikufuna liwapatse ngongole yopanda chikole.

Advertisement