Palibe chifukwa choti tithawe – Usi

Advertisement
Malawi Vice President Michael Usi

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi ogwirizira mpando wa mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) a Michael Usi ati palibe chifukwa choti athawe ntchito yomwe a Chakwera komanso a Chilima anawakhulupilira nayo.

 powasankha kukhala wachiwiri kwa mtsogoleri ndipo ati odumpha azidumpha mu ulendowu.

Poyankhula kwa Kameza mu mzinda wa Blantyre pa ulendo wawo ochokera ku Lilongwe, a Usi ati sadziyankha mu zochitika zambiri monga malemu a Chilima amachitira ngakhale atukwanidwe. 

 A Usi ati ngakhale ena awapekere nkhani, ntchito yawo igona pa kukakoka chitukuko kuti anthu mdziko muno asangalale.

Wachiwiri kwa mtsogoleriyu wati aonetsetsa kuti zomwe analonjeza zitheke ndipo ati mu miyezi ya July ndi August anthu akhale akulandira Chimanga ndi ngongole za NEEF.

A Usi apeleka ulemu kwa a Chilima ndi a Chakwera ponena kuti anthu adabwe chifukwa chani awiriwa anawakhulupilira ndi mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko.

Iwo anaonjezera mmau awo ndi mzembayitso okuti ‘pamene kholo likuphika nsima pamoto nsima ina imadumpha mu nkhali ndi kutayikira pansi koma kholo silisiya kuphika nsima kufikira itapsya’, ndipo iwo ngati kholo apitiliza kuphika kuti aMalawi adye zakupsya.

Iwo ati akhale akufotokozera otsatira chipanichi zambiri mu misonkhano yomwe akhale akupangitsa mu mzinda wa Blantyre ndi maboma ena a ku m’mawa.

Advertisement