Kupilira kwa UTM mu mgwirizano kukanakhala kwa Mazunzo – Chaima

Advertisement
United Transformation Movement (UTM)

Katswiri pa ndale mdziko muno, a George Chaima, ati panali kuthekera koti UTM ipitilire ndi mgwirizano wa Tonse monga momwe anadekhera mtsogoleri wa chipanichi a Saulos Chilima koma ati UTM ikanapilira mozunzika.

Poyankhula mu pologalamu ya ‘Kulinji’ pa wailesi ya Times lero, Katswiriyu wati mzachidziwikire kuti zipani ziwiri za United Transformation Movement (UTM) ndi Malawi Congress Party (MCP) zinali zikulu zikulu mu mgwirizanowu koma mayankhulidwe amene amayankhula a mbali ya chipani cha MCP pena zimawaphinja a UTM,

Katswiri wina Mavuto Bamusi wati Malawi anakhwima pa ndale ndipo ati ndi kofunika kuti pamene ndale zakoma ku Malawi mkofunika kuchita ndalezi mwa mtendere.

A Bamusi anaowonjezera kuti Kusokonekera kwa ubale wa awiriwa kukhudza kwambiri malingaliro ndi chiyembekezo chomwe aMalawi anali nacho pa mgwirizano wa Tonse.

Chipani cha UTM chomwe chinali chimodzi mwa zipani zisanu ndi zinayi 9 zomwe zimapanga mgwirizano wa Tonse chinalengeza kuti chatuluka mu mgwirizanowu ponena kuti izi zikanachitika ngakhale mtsogoleri wawo a Chilima anakakhalapo poti mu mgwirizanowu iwo amanyozedwa komanso samawelengedwa.

Advertisement