UTM yatuluka mgwirizano wa Tonse

Advertisement
United Transformation Movement (UTM)

M’neneri wa chipani cha United Transformation Movement (UTM), a Felix Njawala, ati chipanichi chatuluka mu m’gwirizano omwe unalipo pakati pa chipanichi ndi zipani monga chipani cholamura cha Malawi Congress otchedwa Tonse Alliance.

Izi zanenedwa pa msonkhano wa  atolankhani omwe chipanichi chinakonza ku ma ofesi awo mu nzinda wa Lilongwe masanawa.

Poyankhura pa msonkhanowu, a Njawara anati kuyambira lero, iwo maso awo akhala pa chisankho cha 2025 ngati chipani choyima pachokha.

UTM
Njawala: Tisaope

“A Malawi tiyeni tilembetse mukawundura oponya voti ndi cholinga choti tikwaniritse masophenya a mtsogoleri wathu malemu Chilima.Kuyambira lero ife a UTM tiyeni tisaope, tisafowoke komanso osatopa pamene tikukonzekera chisankho chomwe chikubwerachi”, adatero pototokoza.

Iwo awonjezera pomema a Malawi kuti akalembetse pa mukawundura ncholinga choti azavote komanso kupilidza masomphenya a yemwe anali mtsogoleri wa UTM malemu Saulos Chilima.

M’neneriyi anapempha boma kuti pakuyenera kukhala kafukufuku wapadera ofufuza nkhani ya ngozi ya ndege yomwe inachitika mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba yomwe chifukwa samamvetsabe mpakana lero kuti zinachitika bwanji.

M’mawu ake Mlembi wa chipanichi a Patricia Kaliyati ati akhala ndi msonkhano waukulu umene chipanichi chidzachititse pa 19 mwezi omwe uno komanso mapemphero a misa a padera omwe azalengeze masiku akubwerawa.

Pa msonkhanowu, wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi yemwe anali wachiwiri wa mtsogoleri wa UTM sanakhale nawo.

Advertisement