Bungwe la German Federal Bureau of Aircraft Accident Investigation (BFU) lomwe posachedwapa linatumiza akatswiri ake kudzafufuza za ngozi ya ndege, lati mwezi wa mawa (August) lidzatulutsa zotsatira zoyamba za kafukufuku wake.
Bungwe la BFU lomwe ndilochokera m’dziko la Germany lalemba pa webusaiti yake kuti mkatikati mwa kafukufuku wake lapeza mauthenga ena mothandizidwa ndi makina a makono a GPS.
Bungweli lati izi ziwathandizira kudziwa momwe inayendera ndegeyi yomwe inapha yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino malemu Saulosi Chilima ndi ena asanu ndi atatu pa 10 June 2024.
BFU yati, “Pakafukufuku wa ngoziyi, Global Positioning System (GPS) idapezeka ndipo idatumizidwa ku BFU. Mu chojambulira cha ku BFU, zambiri zokhudza ngoziyi zitha kuoneka. Izi tsopano ziwunikidwa bwino kwambiri ngakhale kuti zitenga nthawi.
“Mongoganizira chabe, kumapeto kwa mwezi wa August, BFU idzatulutsa lipoti loyamba la kafukufukuyu mu Chijeremani komaso mu Chingerezi kudzera pa webusaiti yake.” BFU yatero.
Bungweli lati lipoti loyambali lidzabweretsa poyera mfundo zomwe zasonkhanitsidwa zokhudza ngoziyi kufika pano. BFU yatiso likatuluka lipoti loyambali, idzatulutsanso zotsatira zina momwe mwazina idzabweretsa poyera zomwe zinayambitsa ngoziyi.
Patsikuli la ngoziyi, malemu Chilima ndi ena asanu ndi atatu, anakwera ndege ya asilikali ya mtundu wa Do228-202(K) pomwe amapita ku Nkhatabay ku maliro a Ralph Kasambara