Matako, ndi ena awiri, awapeza olakwa


Matako

Bwalo la Senior Resident Magistrate Joshua Nkhono, ku Balaka lapeza olakwa a Lilian Matako komanso a Ishmael Chitete pa mlandu ovulaza munthu.

Anthu atatuwa akuwaimba mlandu ovulaza mwana wa zaka 9, Mercy Magombo, yemwenso ndi mwana wa mayi Matako.

Powonekera kachiwiri mu bwalori lero masana, oganizilidwawa anavomera mlandu omwe akuimbidwa koma oganizilidwa wina, Zuberi Chitete anawukana mlanduwu.

Bwalori lati lidzapeleka chigamulo chake kwa anthu awiriwa lachinayi pa 18 July, 2024.

Ofalitsa nkhani za apolisi ku Balaka Inspector Gladson M’bumpha wati a Zuberi Chitete akawonekeranso mu bwalori lolemba pa 15 July, 2024 pamene boma lidzabweletse mboni zake pa mlanduwu.

Sponsored

Atatuwa apitililabe kukhala mchitokosi cha Polisi.

Sponsored

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading