Pomwe ena anali ndi chiyembekezo kuti adziyenda shosholo mtaunimu komanso kupanga mathanyura momasuka, pemphero lawo lawomba mgolo pomwe bwalo la milandu lalamula kuti mtchitidwewu ndiosaloledwa kuno ku Malawi.
Lachisanu silinali tsiku wamba, koma lomwe linabweletsa chimwemwe pakati pa atsogoleri amipingo ndi a Malawi ochuluka kamba ka chigamulo cha bwalo la milandu lounika za malamulo pa nkhani ya mathanyula.
Bwalo la milanduli lagamula kuti malamulo a dziko lino apitilirabe kugwira ntchito yopereka chilango kwa amuna kapena akazi ochita ubwenzi komanso kugonana okhaokha.
Chigamulochi chikubwera kutsatira kumang’ala kwa mzika ina ya ku Netherlands a Jan Willem Akster komanso mzika ya m’dziko lino a Jana Gonani omwe amafuna kuti mathanyula akhale ololedwa m’dziko muno.
Awiriwa anakadziwa anakaphika therere kamba koti oweruza milandu Joseph Chigona watemetsa nkhwangwa pa mwala kuti ukwati komanso kugonana amuna kapena akazi okhaokha nkosaloledwa m’dziko la Malawi.
Popeleka chigamulochi munzinda wa Blantyre, oweluza milandu Chigona wati pansi pa malamulo a dziko lino, anthu ochita mchitidwe okwatirana amuna kapena akazi okhaokha apitilirabe kumangidwa komanso kulandira chilango.
Nkhaniyi yasangalatsa magulu ochuluka kuphatikiza azipembedzo. Mwachitsanzo bungwe la Episcopal Conference of Malawi (ECM) kudzera kwa mtsogoleri wake, Archbishop George Desmond Tambala, wati chigamulochi ndichokondweletsa zedi.
Archbishop Tambala wapempha anthu m’dziko muno kuti apitilile kuteteza chikhalidwe chawo ndipo akanitsitse kutengera zikhalidwe za chilendo kuphatikiza kugonana amuna kapena akazi okhaokha.