Atsogoleri a mipingo m’dziko muno ati ndi okondwa ndi chigamulo chomwe bwalo lalikulu la milandu lapeleka lero, kuti malamulo a dziko lino akhale chikhalire ndipo adzipelekabe chilango malinga ndi malamulo kwa anthu ochita m’chitidwe ogonana akazi kapena amuna okhaokha.
Mlembi wa mpingo wa CCAP, Nkhoma Synod, a Vasco Kachipapa, ati ndi okondwa ndi chigamulo chomwe bwalo la milandu latulutsa ponena kuti zimakhala zodabwitsa kumva kuti anthu ena akuchita zinthu zosemphana ndi chilengedwe zomwe n’zosemphananso ndi malamulo a Mulungu.
Iwo ati m’chitidwewu sukuyenera kuloledwa mu dziko lowopa Mulungu.
M’modzi mwa akuluakulu a chipembedzo cha chisilamu, a Shaibu Abdullahan Ajasi, ati dziko la Malawi lero ndi lomwe lapambana popeza lapeleka chigamulo chokomela ilo lomwe ponena kuti chiloweleni nkhaniyi mu bwalo la milandu, anali nayo chidwi nkhaniyi kuti awone chitsogolo chake popeza chipembedzo cha chisilamu chimakanilatu zimenezi, zomwe iwo ati ndi za nyasi.
Odandaula awiri a Jan Willem Akster ndi a Jana Gonani, adakamang’ala ku bwalo lalikulu la milandu kuti liwunike malamulo okhudza zogonana amuna kapena akazi okhaokha ponena kuti malamulo a dziko lino m’mene alili pakadali pano akuphwanya ufulu wa amene amakhala ndi chilakolako chogonana akazi kapena amuna okhaokha, zomwe oweluza milandu atatu awakanila pempho lawoli.