Ngati njira imodzi yokopera alimi kuti akagulitse chimanga chawo ku bungwe logula ndikugulitsa mbewu la ADMARC, bungweli lakweza mtengo omwe likugulira chimanga.
Malingana ndi chi kalata chomwe tawona, bungweli lidzigula chimanga pa mtengo wa K700 pa kilogalamu imodzi, kuchoka pa K650 pa kilogalamu imodzi.
Izi zikutanthauza kuti bungweli pano lidziwagula alimi thumba lolemera ma kilogalamu 50 pa mtengo K35,000 kuchoka pa mtengo wa K32,500 pa thumba lolemera 50 kilogalamu omwe boma linakhazikitsa chaka chino.
Kuwonjezera apo, bungweli lalengezaso kuti alimi amene adzikhala ndi chimanga chochuluka ma tani khumi kapena kupitilira pamenepo (10 metric tons), lidziwagula chimangacho pa mtengo wa K720 pa kilogalamu imodzi.
Izi zikuchitika pomwe malipoti akusonyeza kuti alimi ambiri akugulitsa chimanga chawo m’misika yosavomelezeka (kwa mavenda) komwe akuti akumagulidwa pa mtengo okwelerako kuyelekeza ndi mtengo wa ADMARC.