Ine ndinakagonjetsa a Mutharika ku convention – Nankhumwa

Advertisement
Kondwani Nankhumwa -PDP

A Kondwani Nankhumwa omwe ndi mtsogoleri wachipani cha People’s Development Party (PDP) ati ankapingidwapingidwa m’mene iwo anali membala wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) kamba koti mamembala ena mchipanichi amazindikila kuti iwo akagonjetsa a Peter Mutharika mwayi opita ku msonkhano waukulu okasankha atsogoleri m’ma udindo ukapezeka.

Iwo adayankhula izi pa bwalo la Masintha mu nzinda wa Lilongwe pamene amachititsa msonkhano wokhazikitsa chipani chawochi atawachotsa mu DPP.

A Nankhumwa adati iwo adali chiopsezo kwa anthu ena m’chipanichi nchifukwa chake padapezeka kuti mu chipani muli mpungwe pungwe.

“M’mene ndinali ku DPP ndimaphinjidwa ndi anthu a m’chipanichi kamba koti anthuwa amaopa kuti Nankhumwa akangopita ku convention kokasankha mtsogoleri wa chipanichi, ndikagonjetsa a Peter Mutharika,” anatero a Nankhumwa.

Iwo adapitiliza kunena kuti mpungwepungwewu udafika poipa mpaka iwo adachotsedwa mchipanichi mu January chaka chino.

Pokambapo pa zomwe chipani chawo chidzachite chikadzalowa m’boma, a Nankhumwa anati ndizodabwitsa kuti boma likungophunzitsa aphunzitsi ambiri koma osawalemba ntchito.

Iwo anati boma lawo lidzaonetsetsa kuti aphunzitsi amene amaliza maphuziro awo azidzalembedwa ntchito pompopompo.

“Ntchito zikusowa m’dziko muno kamba koti m’ma ofesi muli anthu ena amene amayenera kupuma pa ntchito koma adakagwirabe ntchito. PDP ikadzangolowa m’boma zonsezi zidzakhala mbiri yakale,” anatero a Nankhumwa

A Nankhumwa anauza ophunzira amene amaliza maphunziro awo msukulu za ukachenjede kuti asiye kumangoombera mmanja zili zonse maka akamauzidwa ndi chancellor wa masukulu aukachenjede kuti akayambitse ma bizinezi akamaliza sukulu.

Iwo anati izi ndizosamveka kamba koti ophunzirawa amakhala alibe mpamba oyambila bizinesi.

“Omwe akuyenera kukayamba ma bizinesi ndi omwe akhalitsa mma ofesimu atenge ndalama zao za retirement akayambe ma bizinesi, ndipo ana omwe amaliza maphunziro m’masukulu aukachenjede akalowe mma ofesiwo,” iwo anatero.

A Nankhumwa anati chipani cha PDP chidzakonzanso nkhani zokhudza chakudya m’dziko muno kamba koti pakadali pano anthu ambiri ali pa vuto la njala chifukwa choti Admarc siikuyendetsa bwino ntchito zake.

“Tidzalemba ntchito ana a sukulu omwe amaliza maphunziro awo ku sukulu ya ukachenjede ya Bunda ndicholinga cholimbikitsa ulimi m’dziko muno,” anatsindika a Nankhumwa.

Iwo anakambaponso za ngongole ya NEEF ponena kuti ali odabwa kuti ndi chifukwa chani akuluakulu ena a boma monga alembi a m’maunduna, nduna zimene ndi ena ambiri akutenga ngongole za NEEF m’malo molora ma venda kuti atenge ngongolezi.

Advertisement