Mwana wamwalira makolo ake atakana kuthamangira naye ku chipatala

Advertisement
Malawi24

Mwana wamwalira ku Zomba makolo ake atakana kumutengera ku chipatala kamba kazikhulupiliro za chipembedzo.

Mwanayu, yemwe ndi wazaka zisanu zakubadwa, anadwala mutu ndipo m’malo mothamangira naye kuchipatala, makolo amwanayu anayamba kumupemphelera kuti achire koma mwatsoka, mwanayu anamwalira.

Bambo amwanayu a Frederick a zaka 46 zakubadwa komanso amayi ake a Fasilen Golosi azaka 38 akusungidwa m’chitokosi cha apolisi ku Zomba kamba kolephera kumutengera mwanayu ku chipatala kuti akalandire thandizo la mankhwala.

Pakadali pano m’neneri wa polisi ya Zomba a Patricia Sipiliano watsimikiza za nkhaniyi.

Banjali limakhala m’mudzi mwa Ramus 2 kwa mfumu yaikulu Ramusi ku Zomba.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.