Apolisi apha oganizilidwa uchigawenga

Advertisement
Malawi24

Apolisi mu mzinda wa Blantyre awombera ndikupheratu munthu wina yemwe akuganizilidwa kuti anapita ku polisi ndikukaba mfuti, zipolopolo ndi utsi okhetsa misozi komaso kuvulaza wa polisi wina m’boma la Chiradzulu.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’dziko muno a Peter Kalaya omwe ayankhula ndi nyumba zina zofalitsa nkhani, munthu ophedwayu wazindikilidwa ngati Mike Banda wa zaka 36.

A Kalaya ati mwezi watha, a Banda anakaba mfuti komanso utsi okhetsa misozi pa polisi ya Nyungwe ku Chiradzulu komweso anavulaza m’modzi mwa apolisi omwe anawapeza patsikulo kenaka ndikuthawa.

Koma poti ukatambatamba umayenera kuyang’ana ku m’mawa kuopa kungakuchere, mkuluyu anamangidwa m’mawa wa Lolemba pomwe anapezeka ndi mfuti yomwe anakaba ku Chiradzulu-yo.

A Kalaya atsimikiza kuti Banda anamangidwa potsatira pachipikisheni chomwe apolisi apansewu anapanga galimoto yomwe mkuluyu anakwera pomwe amalowera ndi mfutiyo m’boma la Chikwawa.

Atapanikizidwa ndi mafuso, iye anaulura kuti mfutiyo anakaiba ku polisi ya Nyungwe m’boma la Chiradzulu ndipo anaulula kuti ali ndi zida zina za apolisi zomweso akuti anakaba ku Chiradzulo-ko. 

Apa Banda anawatengera apolisi m’mudzi wina komwe anafukula zidazo pa malo ena omwe anazikwilira ndipo posakhalitsa iye anayamba kuthawa zomwe zinachititsa apolisi kuti awombe mfuti.

Banda anafera pa malo omwewo ndipo pakadali pano thupi lake likusungidwa ku chipatala cha Queen Elizabeth Central munzinda wa Blantyre.

Advertisement

2 Comments

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.