Bungwe la NICE lilimbikitsa ubale wake ndi Atolankhani 

Advertisement
National Initiative for Civic Education (NICE)

Bungwe loima palokha lophunzitsa anthu Zinthu zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education(NICE) lati ndikofunika kuyendera limodzi ndi atolankhani pakuonetsetsa kuti chilungamo chikuyenda bwino pa nkhani za chitukuko m’madera osiyanasiyana m’boma la Nkhata-Bay.

Poyankhura pa nkumano wa atolankhani omwe bungweli linakonza ku ofesi yawo m’bomali, wamkulu oyang’anira zamapulogalamu ku bungweli mu boma la Nkhata Bay mai Lucy Kalua,  watsindika zakufunika kogwilira ntchito limodzi pakati pa bungwe lawo ndi atolankhani.

Iwo ati, atolankhani ndi maso kamanso mlomo wa anthu ambiri omwe sangakwanitse kudziyimilira paokha ndipo kuti pongwira nawo ntchito limodzi madera ambiri atha kutukuka.

“Inuyo ngati atolankhani muli ndiudindo waukulu posintha dziko ndipo kudzera mukalondolondo yemwe mungamapange zinthu zitha kupezeka kut zikuyenda bwino mumaofesimu ndimumadera.”

Mophera mphongo zomwe Kalua wanena, owona zofalitsa uthenga m’bomali  komanso yemwe ali  oyankhulira Khonolo ya Nkhata Bay wavomelezana nowo ponena kuti nkhani zofufuzidwa bwino ndi chida pachokha popititsa chitukuko patsogolo.

“Mwachitsanzo pano ma khonsolo amalandira ndalama za GESD malingana ndi momwe agwilira ntchito zawo, zonsezi kut zibwele poyera ndinu atolankhani anzanga.”

Poyankhurapo, m’modzi mwa atolankhani  amene anapezeka nawo mu mkumanowu Nobert Mzembe wa wailesi ya Zodiak, wathokoza bungweli pozindikira kufunika kwa atolankhani pakuonetsetsa kuti zitukuko zikuyenda momwe zikuyenera ziyendera.

Mzembe wapitilizanso kulipempha bungweli kuti lidzapezenso nthawi ndikuyitana azitsogoleri kapena anthu amaundindo osiyanasiyana pamodzi ndi atolankhani kuti azadziwe kuti atolankhani si adani koma abale

Pamapeto pa zonse bungwe la NICE linapeleka mpata kwa atolankhani m’bomali kupeleka maganizo awo momwe angagwilire ntchito limodzi pakuonetsetsa kuti pa zitukuko pali chilungamo, ndipo mwa zina atolankhaniwa anatchulapo kuti NICE ikuyenera iziwaganizirako mayendedwe kuti akavumbulutse zitukuko zomwe zikukhalilidwa mumadera ovuta kuwafikira.

By Felix Kamanga

Advertisement