Ophunzira okwana 17 ochokera pa sukulu ya pulayimale ya Chawe m’boma la Chiradzulu, ali manja m’khosi pomwe zadziwika kuti salemba nawo mayeso a sitandade 8 kamba koti mphunzitsi wina pa sukuluyi anawadyera ndalama yolipilira mayesowa omwe akulembedwa sabata ino.
Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Chiradzulu a Cosmas Kagulo omwe azindikira m’phunzitsiyu ngati Daniel William, wa zaka 36 omwe pano akusungidwa m’chitokosi cha a polisi m’bomali.
A Kagulo ati a William amangidwa powaganizira kuti anawononga ndalama zokwana K67,150 zomwe amayenera kulipilira mayeso a ophunzira a sitandade 8 okwana 17 pa sukulu ya pulayimale ya Chawe.
Ofalitsankhaniyu watiuza kuti mbuyomu, mphunzitsiyu anasankhidwa ndi aphunzitsi anzake pa sukuluyi kuti atolere ndalama zolipilira mayeso kuchokera kwa ophunzira a sitandade 8 ndipo awalipilire ophunzirawa ku bungwe loyendetsa mayeso la MANEB kudzera pa Lamya.
Atatolera ndalama zonse, zadziwika kuti m’phunzitsiyu analephera kudzigwira mtima ndipo anathira pa lilime zina mwa ndalama za ophunzirawa ndipo nkhaniyi yadziwika sabata yangothayi pomwe ophunzira ena sanalandire ziphaso zawo zolembera mayeso.
A polisi ati mayina a ophunzirawa sanali nawo pa ndandanda wa ophunzira omwe akuyenera kulemba nawo mayeso zomwe zinachititsa jenkha aphunzitsi pa sukuluyi ndipo anayamba kufusana kuti chachitika nchiyani.
Mkati mofufuza, zinadziwika kuti m’phunzitsi sanawalipilire ophunzirawa ndalama ya mayesoyi ndipo apa nkhaniyi inakasiyidwa m’manja mwa apolisi omwe sanachedwa koma kuthira dzingwe mphunzitsi oganizilidwayu ndipo atapanikizidwa ndi mafuso, William wavomera kuti anadyadi ndalamazi.
Izi zikuchitika pomwe ophunzira a sitandade 8 m’dziko muno akhala akulemba mayeso awo omwe akuyamba la chitatu pa 22 May mpaka Lachisanu pa 24 May 2024.
Pakadali pano, sipanapezeke njira yoti anawa alembebe mayesowa kamba koti sivuto lawo.