NRB yatsimikizira aMalawi kuti ikugwira ntchito yake mwa ukadaulo

Advertisement
NRB

Bungwe loyendetsa kalembera m’dziko muno la National Registration Bureau (NRB) lati ilo likupitilira kugwira ntchito yake mwaukadaulo ngakhale pali madandaulo kuchokera kwa mzika zina zokhudzidwa kuti kalemberayi sakuyenda bwino.

Izi zadza pamene gulu la mzika zokhudzidwa zati pali andale ena omwe akumauza ana omwe sanakwane zaka 16 kuti akalembetse mukaundula ndicholinga choti adzavote mu chisankho cha chaka cha mmawa.

Muchikalata chomwe bungweri latulutsa pa za nkhaniyi lati ilo ndilokhudzidwa ndi mphekesera zomwe gulu la mzika zokhudzidwazi lafotokoza zoti ana osakwana zaka 16 akulembetsa mu kaundula wa umzika kudzera mu ntchito yolemba anthu mkaundulayu yomwe ikuchitika m’madera.

NRB yati gawo 43 la malamulo a kalembera wa umzika, munthu aliyense amene wapereka mbiri yake yabodza polembetsa m’kaundula komanso wapeleka umboni wabodza ndi cholinga cholembetsa m’kaundula komanso ngati mu njira ina iliyonse akufuna kupusitsa mkulu wa kalembera kuti amulembe m’kaundula; amakhala wapalamula mlandu.

Bungweli lati chilango cha milanduyi ndi kupereka chindapusa cha ndalama zokwana K1,000,000 ndi kukakhala ku ndende zaka zisanu.

Bungweli lapempha guluri kuti lipereke umboni wa nkhaniyi ku bungweli kuti nalonso lifufuze palokha za nkhaniyi.

Ilo lati zomwe mzika zokhudzidwazi zanena ndi mlandu waukulu, ndipo bungwe la NRB likuyenera kuchitapo kanthu.

NRB yapempha mzika zokhudzidwazi kuti zikatule madandaulowa kwa a Polisi m’dziko muno kuti afufuze za nkhaniyi ndipo NRB yatsimikizira a Malawi kuti madandaulo omwe gulu la anthu okhudzidwawa lapereka alitsatira bwinobwino mpaka kumapeto ndipo a Malawi adziwitsidwa zotsatira zake.

Malingana ndi m’tsogoleri wa mzika zokhudzidwazi, a Wells Khama, anthu andale akumauza ana omwe sanakane zaka 16 akalembera ndi kukanama kuti ali zaka 18 kapena kuposera apo ndicholinga choti adzakwanitse kuvota chaka cha mawa.

A Khama ati iwo atafufuza apeza kuti anthu andalewa akumawapatsa anawa ndalama kapena kuwaika mndondomeko ya Social Cash Transfer.

Advertisement