Ngati wina kundendeko amakonzekera kuti tsiku lina adzakhala mesho wa a Saulos Chilima asiyiletu. Milandu yawo yonse ija a boma aithetsa. Tsopano ndi mfulu.
Bwalo la milandu lero pa 6 May lavomereza pempho lochoka kwa mkulu oyimba milandu oti milandu ya katangale yokhudza wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ithe. Izi zili mu chikalata chimene Malawi24 yaona pa makina a Intaneti.
Malinga ndi chikalatachi, mkulu ozenga milandu ya boma a Masautso Chamkakala adziwitsa bwalo kuti iwo tsopano sapitilizanso kuyimba milandu a Chilima ndipo a bwalo awamasule basi akhale ngati mfulu.
Monga mwa lamulo, a Chamkakala sanafotokoze ndi komwe zifukwa zake zomwe athetsera mlandu.
Kuthetsa mlandu wa Chilima kwadza pamene a Chilima adapempha mu bwalo kuti iwo apatsidwe mwayi ogwiritsa ntchito zikalata zochokera kwa asilikari ngati umboni mu nkhani yawo. A bwalo adachita jenkha ponena kuti izi zinali ndi kuthekera kosokoneza chitetezo cha dziko.
Koma ena mwa a Malawi akhala akukayika kunena kuti bwalo linakhalila umboniwu kamba koti umatchula mtsogoleri wa dziko.
Imeneyi idakali kuwanda ndi pamene basi a boma alengeza zoti athetsa milandu ya a Chilima.
A Chilima adanjatwa poganiziridwa nkhani zokhudzana ndi katangale ndi namatetule wa za malonda a Zunneth Sattar. Mwa zina iwo ati anapangitsa kuti ku likulu la asilikari mu dziko muno apereke ma kontalakiti kwa a Sattar mwa chinyengo.