Mayunitsi okala akuthetsedwa m’dziko muno

Advertisement
Mobile-Phone

Zadziwika kuti mayunitsi a lamya okhala pa khadi lija limachita kukalidwa lija, akhala akuthetsedwa mdziko muno sabata ya mawa ino.

Izi zikutsatira mikumano yomva maganizo a anthu yomwe bungwe lowona za nkhani zolumikizana la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lakhala likuchititsa mbuyomu pa nkhaniyi.

Potsatira nkhaniyi, bungweli laitanitsa msonkhano wa atolankhani omwe uchitike pa 30 April, 2024 ku Lilongwe komwe likuyembekezeka kukathetsa mayunitsi okalawa komaso kufotokoza momwe kugula mayunitsi a lamya kudzikhalira.

Malingana ndi kalata yomwe wasainira mkulu wa bungwe la MACRA, a Daud Suleman yoyitana atolankhani ku nsonkhanowu, kuthetsa mayunitsi okalawa kuthandiza dziko lino pa zinthu zingapo.

“Monga mukudziwira, bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) lakhala likukambirana ndi anthu okhudzidwa pakufunika kothetsa kugwiritsa ntchito mayunitsi okala m’Malawi.

“Kutsatira zokambirana za magulu okhudzidwa pa nkhaniyi, ndikufuna kukudziwitsani kuti bungweli lavomereza kuthetsa kugwiritsa ntchito makadi powonjezera mayunitsi mu foni,” yatelo mbali ina ya kalatayi yomwe yalembedwa mchingerezi.

Kalatayi yati iyi ndi imodzi mwa ntchito zomwe boma la Malawi likuchita pofuna kulimbikitsa ntchito za malonda za makono m’dziko muno zomwe cholinga chake ndi kupititsa patsogolo ntchito zochita malonda popanda kugwiritsa ntchito ndalama za pepala.

Bungweli lati ubwino winanso wothetsa mayunitsi okalawa ndi oti makampani a lamya ayamba kupulumutsa ndalama zomwe amagwiritsa ntchito akamagura ma khadi opangira mayunitsiwa kuchokera mayiko a kunja.

Bungwe la MACRA latiso ntchitoyi ithandizanso kuteteza chilengedwe m’dziko muno.

Advertisement