Anthu atatu agwidwa atapezeka ndi Chamba kwa Jenda ku Mzimba

Advertisement

A Polisi akwa Jenda m’boma la Mzimba amanga anthu atatu atawapeza ndi Chamba mdera la Luviri chomwe amafuna apite nacho ku Lilongwe.

Mneneri wa a polisi ya Jenda, Sub Inspector Macfarlen Mseteka, wawuza Malawi24 kuti anthuwa adagwidwa akufufuza mayendwe wopita ku Lilongwe mpomwe anthu adatsina khutu a Polisi mderalo.

Womwe apalamula mlanduwu ndi mayi Pilirani Phiri azaka 46 ndi amuna ena awiri Stanely Mologeni, 34, ndi Ryford Wagiwa, 37, omwe adawapeza ndi mabeseni 10 achamba, ndipo adawazembanitsa ngati atenga tomato.

“Chamba china chinali mmatumba cholemera makilogalamu 21, ndipo mnzawo wina anakhwanitsa kuthawa atasiya kachikwama konyamuliramo laputopu muli chamba cholemera makilogalau asanu,” atero a Mseteka.

Anthuwa awatsegulira mlandu wopezeka ndi chamba wopanda chilolezo, ndipo akuyembekezeka kukayankha mlandu, kufufuza kukamalizika.

A Polisi akuyamika anthu kamba kowathandiza kuthana ndi mchitidwe wopalamula, ndipo akuchenjeza anthu kuti kupezeka ndi chamba opanda chilolezo ndi kuphwanya malamulo adziko lino.

Phiri amachokera m’boma la Phalombe, Mologeni ku Dedza pomwe Wagiwa amachokera ku Thyolo ndipo onsewa amapanga malonda awo mu mnzinda wa Lilongwe.

Advertisement