Pali chiyembekezo choti chiwerengero cha anthu otenga kachilombo ka HIV chitha kuchepa mdziko muno kamba koti unduna wa zaumoyo walengeza kuti PrEP wobaya yemwe amathandiza kuchepetsa chiopsyezo chotenga kachilombo ka HIV, wayamba kupelekedwa mzipatala zina ku Lilongwe komaso Blantyre.
Izi ndi malingana ndi kalata yomwe undunawu watulutsa Lamulungu pa 24 March, 2024 yomwe wasainira ndi mlembi wankulu ku undunawu Dr Samson Mndolo, yomwe yati ntchito yopeleka mankhwalawa yayamba kaye pa zipatala zitatu ku Blantyre komaso zitatu ku Lilongwe.
Undunawu wati kuyamba kupeleka PrEP obaya kukutsatira kukhazikitsidwa kwa ndondomekoyi mu chaka cha 2023 m’boma la Lilongwe ndipo wati mankhwalawa akuperekedwa kaye muzipatala zochepazi kuti undunawu uwone kuti ntchitoyi iyenda motani komanso anthu ayilandira bwanji, PrEP wobayayu asanayambe kuperekedwa mu zipatala zina 41 m’dziko lino.
“Unduna wa Zaumoyo ukudziwitsa anthu kuti tsopano ukupereka PrEP wobaya wothandiza kuchepetsa chiopsyezo chotenga HIV mdziko la Malawi lino m’zipatala zitatu ku Blantyre (Chilomoni Health Centre, Limbe MACRO ndi Naperi Drop in Centre) komanso zipatala zitatu ku Lilongwe (Area 25 Health Centre, Chipatala cha Bwaila ndi Area 47 Drop in Centre), yatelo mbali ina ya kalatayi.
Undunawu wati uli ndi chiyembekezo kuti ntchito yopeleka PrEP obayayu ithandiza kukwanilitsa masomphenya othana ndi ka chilimbo ka HIV pofika chaka cha 2030 ndipo watiso dziko lino lapita patsogolo pomwe kafukufuku akusonyeza kuti chiwelengero cha anthu omwe ali ndi HIV chatsika kwambiri kuchoka m’chaka cha 2016 kufika mu 2021.
Ngakhale zili choncho undunawu wati HIV ikupitilirabe kufala m’magulu ena omwe ali pachiopsyezo chachikulu chotenga HIV monga azimayi oyendayenda, atsikana komanso achinyamata, amayi oyembekezera komanso oyamwitsa ndipo wati ndi chifukwa chake yabweretsa PrEP obaya kuti HIV isapitilire kufala.
Kupatula apo, undunawu walimbikitsaso anthu kuti apitilire kugwiritsaso njira zina zomwe undunawu ukupeleka zopewera HIV m’zipatala za boma zomwe ndikuphatikizapo PrEP wakumwa, makondomu, PEP, mdulidwe wa abambo wa kuchipatala, komaso kupewa kufala kwa HIV kuchoka kwa mayi kupita kwa mwana.
Unduna wa Zaumoyo wati PrEP wobaya akhoza kupelekedwa kwa wina aliyense amene wakwanitsa zaka 15 kapena kuposera apo amene alibe ka chilombo ka HIV koma ali pachiopsyezo chachikulu chotenga kachilomboka ndipo wati mankhwalawa si katemela wa HIV.
“Dziwaninso kuti PrEP wobaya sikatemera wa HIV ndipo sapereka chitetezo kwa munthu ngati ali kale ndi HIV, komanso sateteza munthu ku matenda opatsirana pogonana. Kuti mudziwe zambiri, chonde khalani omasuka kulankhula ndi a Unduna wa Zaumoyo ku Dipatimenti ya HIV, Edzi ndi Viral Hepatitis kapena ku Health Promotion Division ndi National AIDS Commission (NAC),” yatelo so mbali ina ya kalatayi.
Undunawu waonjezeraso kuti PrEP wobayayu akuperekedwa ndi thandizo lochokera kumabungwe monga U.S. President’s Emergency Plan for AIDS Relief, Bill and Melinda Gates Foundation komanso a Center for Innovation in Global Health yaku Georgetown University.