Bambo amangidwa kaamba kovulaza wakuba

Advertisement

Apolisi ku Namwera m’boma la Mangochi amanga Abdullah Nandi wa zaka 38 kaamba kovulaza mnyamata wina Major Majid wa zaka 20 yemwe amamuganizira kuti anamubera m’munda mwake.

Mneneri waapolisi ya ku Mangochi, Amina Tepani Daudi, wati izi zinachitika mmawa wa Lamulungu pomwe Nandi anagwira wakubayu.

Mneneri wa Police yu wati Iwo adadziwa zankhaniyi ataona kanema yemwe anatuluka pa masamba a mchezo ndipo poona izi apolisi adapita kukamanga a Nandi.

A Daudi anati Nandi adamangilira Majid pa galimoto yake ya Ford Courier ndikumukokera munsewu atamugwira akuba tomato.

Ndipo atafika pa mphambano yomwe ili pafupi ndi msewu wa phula, anthuwa anamasula Majid poopa kuti anthu angawawone koma Majid anali atasupuka kwambiri ndipo anamutengera pa chipatala cha Namwera kuti akalandire thandizo.

Pakadali pano, apolisi m’bomalo alangiza anthu kuti asatengere lamulo m’manja mwawo pofuna kupewa milandu ngati imeneyi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.