Bushiri wagawa chimanga kwa anthu 18,000 ku Lilongwe

Advertisement
Bushiri wagawa chimanga kwa anthu 18,000 ku Lilongwe

Pomwe akupitilira ndi ntchito yogawira chimanga anthu omwe akhudzidwa ndi njala m’dziko muno, mtsogoleri wa mpingo wa Enlightened Christian Gathering (ECG), Mneneri Shepherd Bushiri, wagawa chimanga kwa anthu opitilira 18,000 munzinda wa Lilongwe.

Mneneri Bushiri wagawa chimangachi Lamulungu pa 17 March, 2024 kulikulu la ofesi yake ku Golden Peacock mu mzinda wa Lilongwe komwe khwimbi la anthu linakhamukira ndicholinga chofuna kukalandira chakudyachi kuti kwa masiku angapo, awone pogwira.

Poyankhula ku zikwi zikwi za anthu omwe anali mbwee pamalopa, Mneneri Bushiri wati ndi okondwa kuti ntchito yogawa chimangachi kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala mdziko muno, ikuyenda bwino.

Iwo anabwerezaso kulimbikitsa anthu komaso makampani akufuna kwa bwino kuti agwirane nawo manja kuti apulumutse miyoyo ponena kuti ntchitoyi siyikufunika kusiyirana kamba koti omwe akufunikira thandizo la chakudya ndi anthu ambiri.

“Ndine osangalala kuti anthu ambiri alandila nawo thandizoli ndipo ndikulimbitsa onse akufuna kwabwino kuti tigwirane manja populumutsa miyoyo ya a Malawi anzathu omwe akuvutika ndi njala. Ndi udindo wa aliyese kutenga nawo gawo pa nkhani yopulumutsa miyoyo ya a Malawi anzathu,” watero Mneneri Bushiri.

Ambiri mwa anthu omwe anafika kudzalandira thandizoli, anali ochokera m’madera monga Kauma, Chilinde, Kawale, Senti, Chimoka, Mtandire ndi ena ambiri.

Pakadali pano anthu am’maboma a Mzimba, Karonga, Nkhotakota, Ntcheu, Lilongwe, Rumphi, Mulanje, Thyolo, Zomba, Nsanje ndi Nkhatabay ndi omwe alandira thandizoli, ndipo ntchitoyi ikhala ikupitilira m’ma boma ena komwe njala yafika posauzana kwambiri.

Kumayambiliro kwa mwezi watha, Mneneri Bushiri anakhazikitsa ntchito yogawa chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndi njala m’dziko muno chomwe akuti ndi cholemera ma “metric tons” 17,000 chomwe akuti ndi cha ndalama zosachepera 14 biliyoni kwacha.

Advertisement