Nthambi Yoona Zanyengo m’dziko muno yati chiyembekezo choti mpweya opepuka omwe uli mu nyanja ya mchere ya Indian Ocean usanduka namondwe chachepa.
Nthambi yi yati namondweyo saakuyembekezekanso kubadwa m’masiku atatu akudzawa komabe mpweya opepukawu ukhala ukuyendabe panyanjayi koma ndizokayikitsa kuti ufika m’dziko lino.
“Ngakhale izi zili chonchi, mpweyawu ulimbikitsa kugwa kwa mvula m’madera ambiri m’chigawo cha kummwera kuyambira madzulo a Lamulungu pa 10 March mpaka Lachitatu pa 13 March, zomwe zingadzetse kusefukira kwa madzi,” yatero nthambiyi.
Ndipo Nthambiyi yati maboma omwe angakhudzidwe kwambiri ndi mvulayi ndi a Nsanje, Chikwawa, Chiradzulu, Mulanje, Phalombe, Blantyre, Mwanza komanso Thyolo.
Ndipo madera omwe ali ku Zomba komanso Neno akuyembekezeka kukhudzidwa mocheperako.
“Pachifukwachi, Nthambi Yoona za Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi ikupitirizabe kupempha kuti titsatire malangizo monga kusamukira mmadera a kumtunda, kuonera, kumvera komanso kuwerenga uthenga wa za nyengo kuti tidziwe momwe nyengo ikhalire m’dera lathu,” yaonjezera motero Nthambi yi.
Nthambi yi yapemphanso anthu kuti apewe kuoloka mitsinje yosefukira komanso kuyenda m’madera omwe madzi asefukira ndipo yaonjezera kunena kuti madzi angachepe bwanji, ali ndi kuthekera kokokolora.
“Tisayandikire mawaya a magetsi, tidziwitse msanga a ESCOM, amfumu kapena a polisi za mawaya kapena mapolo a magetsi omwe agwa,” yatsindika motero Nthambiyi.
Nthambiyi yapempanso anthu kuti asamutsiretu katundu yense wofunikira ku malo okwera.