Boma likufuna kuti anthu 50 pa 100 aliwonse azakhale ndi magetsi pofika 2030

Advertisement

Unduna woona mphamvu za magetsi m’dziko muno wati boma likufuna kuti pofika chaka cha 2030, anthu 50 pa anthu 100 aliwonse adzakhale akugwiritsa ntchito magetsi.

Pakali pano anthu 27 pa anthu 100 aliwonse ndi amene akugwiritsa ntchito magetsi m’dziko muno.

Mlembi wamkulu mu undunawu Alfonso Chikuni ndiye watsimikiza izi ndipo wati lingaliloli lidzatheka chifukwa unduna wawo ukufunitsitsa kulumikiza magetsi kwa anthu 250,000 kwa chaka chilichonse Kufikira chaka cha 2030.

Chikuni anayankhula izi ku BICC mu mzinda wa Lilongwe lero pamene nduna ya za migodi Monica Chang’anamuno amatsekulira gawo lachiwiri lokonza mphamvu za magetsi kuchokera kuchilengedwe lokonzedwa ndi bungwe la Presidential Delivery Unit-PDU.

“Kupita patsogolo ndi ntchito yokonza mphamvu za magetsi kukhala kovuta chifukwa cha kuchuluka kwa anthu omwe akufuna magetsi.

“Mwachitsanzo, Nthambi ya migodi imagwiritsa ntchito magetsi oposera 230 megawatsi,” anatero a Chang’anamuno.

Mkulu wa Bungwe la PDU, Janet Banda, yemweso ndi wachiwiri kwa mlembi mu ofesi ya tsogoleri wa dziko lino, wati ntchitoyi ikukhala yovuta chifukwa cha zotsamwitsa zimene akukumana nazo koma boma likuyesetsa kupeza njira zothana ndi mavuto omwe akumana nawo ndi cholinga chofuna kupititsa pa tsogolo ntchitoyi m’dziko muno.

Mu mau ake, mkulu wa bungwe la Global Energy Alliance for People and Planet lomwe likuthandizira boma kupititsa pa tsogolo ntchito yokonza mphamvu za magetsi kuchokera ku chilengedwe, Collen Zalengera, wati ali ndi chikhulupiriro kuti tchitoyi ipitilira ndipo isintha miyoyo ya a Malawi ambiri.

Wolemba : Peter Mavuto

Advertisement