Tiyeni timenyebe nkhondo yolimbana ndi mavuto a zachuma, watero Tobias

Advertisement
Milward Tobias is a Malawian presidential aspirant

Mtsogoleri wa chipani cha Mzika Coalition, Milward Tobias, wapempha a Malawi kuti asatope pofuna kuthana ndi mavuto a zachuma omwe ali mu dziko muno.

Izi zayankhulidwa pamene dziko lino likukumbukira amatiliti amene anamenyera ufulu kuti dziko lino kuti likhale loima palokha.

Mu chikalata chomwe watulutsa, Mtsogoleriyu wati dziko lino likuyenera kukhala  ndi chidwi kwambiri pakumanga Malawi amene adzapindulire mibadwo mibadwo ya tsogolo.

A Tobias ati: “M’malawi aliyese akuyenera kuganizira njira yoyenera yosinthira zinthu m’dziko muno ndipo ndikuonenetsa kuti njirayo yakwanilitsidwadi.”

Oyankhulapo pa m’mene boma likuyendera boma, Wonderful Mkhutche, wati tsikuli likumbutse a Malawi kuti ufulu odzilamulira patokha sunapatsidwe kwa ife mophweka.

“Ngati a Malawi, tizindikire kuti abale athu anadzipereka msembe kuti ife tipeze ufulu odzilamulira, koma nthawi zina timaiwala kumene tachokera ndi kumene tikupita ngati dziko,” anatero a Mkhutche.

Mwambo okumbukira amatiliti chaka chino unachitikira m’dera la mfumu yaikulu Mkumbira M’boma la Nkhata-Bay ndipo mtsogoleri wa dziko lino ndi akuluakulu ena a boma anatenga nawo mbali pa mwambowu.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement