Anthu kudera kwathu akufuna mtsogoleri wachinyamata komanso wamasomphenya — atero a Chipenembe

Advertisement

Yemwe akufuna kudzayimira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) m’dera la Chiradzulu Masanjala pa zisankho za 2025 a Rockie Chipenembe, awuza Malawi24 kuti ku dera kwawo anthu akufuna iwowo kuti akhale Phungu, chifukwa ndi wachinyamata komanso ali ndi masophenya zomwe zingathandizile kutukula deralo.

Malingana ndi a Chipenembe, kudera kwawo kukupelewela zinthu zambiri komanso anthu ambiri akukhala moyo wovutika ndipo iwowo akazawina azawonetsetsa kuti mavuto onse omwe anthu amu deramo akukumana nawo azathe. Iwo anawuzaso Malawi24 kuti anthu aku Chiradzulu Masanjala pofuna kuti zinthu zisithe mu deralo, agwilizana zoti 2025 avotere iwowo ngati Phungu wa deralo.

Chipenembe akulonjeza zitukuko zochuluka.

“Ndikufuna ndikonze zinthu ngati izi mu dera lathu, Chitetezo chonkhwima Ku anthu a derali makamaka kuthetsa zaupandu, kuwononga zinthu zachilengedwe zithe. Ndikufuna Kuwonetsetsa kuti pakhale moyo wotetezeka, wamphamvu, komanso anthu azipeza chakudya chotsika mtengo mosavuta.

Kukhazikika kwachuma, kuonetsetsa kuti pali chitetezo kwa anthu a pantchito komanso kuti maufulu awo sakuphwanyidwa, kumanga misewu, milatho, zipatala zing’onozing’ono, masukulu komanso kupeleka ngongole Kwa achinyamata. Izi ndi mwa zina zomwe ndufuna ndibweretse mu derali ndikasankhidwa ngati phungu,” iwo anatero.

Malingana ndi a Chipenembe, chomwe chawapangitsa kuti aganize zodzapikisana nawo pa u Phungu wa mu derali ndi kuwawidwa mtima chifukwa cha kulephera Kwa atsogoleri omwe akhala akulamulira derali komanso kukanika Kwa atsogoleri wo kupanga zitukuko zolozeka ndi zopindulira anthu.Iwo anenetsa kuti palibe yemwe akumuwopa ku Chiradzulu Masanjala Ku mbali ya opikisana nawo.

Ndipo awamema onse amene akuwonetsa chidwi kuti abwere adzapikisane nawo pa zisankho.

“Ndikuwamema anthu onse amene akuonetsa chidwi kuti abwere tipikisane ndipo okha adzavomeleza kuti mwana wa mudzi wafika ndipo palibe angapikisane naye,” iwo anatero.

Advertisement