Eli Njuchi wati sakupeza bwino ndipo sakhala nawo kumapwando a lero

Advertisement

Eli Njuchi walengeza kuti sakwanitsa kuyimba nawo pamapwando awiri azamayimbidwe omwe akhale akuchitika m’boma la Salima lero pa 1 March komanso mawa pa 2 March munzinda wa Blantyre kaamba kakuti sakupeza bwino.

Katswiriyu wanena izi kudzera mumkalata yomwe iye watulutsa kudzera pa tsamba lake la mchezo la Fesibuku.

Eli Njuchi pakadali pano sakupeza bwino.

Njuchi wati akupepesa kamba kakulephera kuyimba nawo pa malo awiliwa ndipo iye wati izi zili chonchi kamba kakuti madotolo amulangiza kuti apume kaye.

Iye amayenera kukakhala nawo kumapwando awili azamayimbidwe omwe akhale akuchitika lero mboma la Salima pa Culture Club komanso munzinda wa Blantyre ku Beerland.

Advertisement