Siyani musatchetcheso chimanga kuli njala – boma lauza khonsolo ya Lilongwe

Advertisement

Boma kudzera ku unduna owona za maboma aang’ono, umodzi komanso chikhalidwe lauza khonsolo ya Lilongwe kuti isiye ntchito yotchetcha chimanga chomwe chili m’malo oletsedwa ponena kuti kunjaku muli kale chiopsezo cha njala.

Pomwe m’dziko muno muli kale chiopsezo cha njala yadzaoneni, anthu Lachitatu anadzidzimuka kuti akuluakulu a khonsolo ya Lilongwe anatuma ogwira ntchito awo kukatchecha chimanga chomwe chinadzalidwa m’malo oletsedwa m’madera ngati ku Area 43 ndi Area 11 munzindawu.

Koma boma kudzera ku unduna owona za maboma ang’ono, umodzi komanso chikhalidwe lati lamva madandaulo omwe anthu apereka pa nkhaniyi ndipo lalamula akuluakulu a khonsoloyi kuti stayed zisenga zonse ndipo ntchito yotchetcha chimangachi iyimitsidwe kaye.

Izi ndi malingana ndi kalata yomwe undunawu watulutsa lachinayi yomwe wasainira ndi mlembi mu undunawu a James Chiusiwa omwe ati ganizoli labwera polingalira kuti dziko lino lili kale pachiopsezo choti chimanga chitha kukhala chochepa kamba ka kuvuta kwa mvula.

“Unduna wa maboma ang’onoang’ono, mgwirizano ndi chikhalidwe, ukufuna kudziwitsa anthu onse kuti wamva madandaulo okhudza zomwe khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yachita pa 28 February, 2024 potchetcha mbewu ya chimanga yomwe imabzalidwa m’malo okhala anthu a Area 43 ndi 11.

“Undunawu wazindikira kuti anthu ambiri akuyamikira kuti ntchitoyi idachitika motsatira malamulo omwe adalipo kale, koma anthu akukhudzidwa ndi nthawi yomwe ntchitoyi yachitika poganizira za mlingo omwe mbewuzi zinali komanso mavuto omwe akuyembekezeredwa pa kakololedwe ka chimangacho chaka chino. Choncho unduna uno wakambirana ndi khonsolo ya mzinda wa Lilongwe kuti iyimitse ndikuwunikanso nthawi yochitira ntchitoyi,” yatelo kalatayo.

Ngakhale zili choncho, undunawu sunafotokoze kali konse pa zomwe zikuyembekezera kuchitika kwa ma banja omwe atchetcheledwera chimanga chawo kamba koti zikumveka kuti khonsoloyi inali itatchetcha kale minda yokwana khumi (10).

Advertisement