Osangolimbikira kubeleka ana oti simungawasamale — Chakwera

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati ndi nthawi yabwino tsono kuti makolo azindikire za ubwino okhala ndi ana omwe akhoza kukwanitsa kuwasamala komanso kuwaphunzitsa ndipo ati maphunzilo kuti ayende bwino akuyambila pa zipangizo, ma kalasi abwino, aphunzitsi okwanila komanso kuphatikiza udindo omwe makolo ali nawo.

Poyankhula pa sukulu ya pulayimale ya Chikololere ku m’mawa kwa boma la Dedza pamene amatsekulira ntchito yomanga zipinda zophunzilira zokwana 10,900 ndi zipinda zosinthira atsikana zokwana 1,000, a Chakwera anati chilimbikitso cha makolo kuti ana awo apite ku sukulu ndi ngodya yachinayi pa maphunziro.

‘Belekani ana oti mukwanisa kuwasamalira’- Chakwera.

Mtsogoleriyu wati boma likhonza kupanga zonse zothekera kuti maphunziro ayende koma ngati makolo akungochilimika kubeleka ana kulephera kuwasamalira komanso kuwaphunzitsa osatumiza ana ku sukulu ndi kuwalimbikitsa ana awo zonse zili chabe maka ana a chitsikana.

“Aliyense pakhomo osangolimbikira kubeleka ana oti sungawasamalire mkuwaphunzitsa mkomwe ayi, kumanena kuti awasamalira amalume awo ayi, ngati muli adindo mukuyenera kukhala adindo a banja lanu” atsindika a Chakwera

Mtsogoleriyu wati masomphenya a dziko lino a 2063 sangakwanile opanda ana amene pakali pano Ali ku pulayimale ndipo a Chakwera atsindika kuchilimika kugwira ntchito yothandizira kukwanilitsa masomphenya kuthandiza ana potengela kuti ambiri m’dziko muno pa chiwelengelo ndi ana a ku pulayimale.

A Chakwera atsekulira ntchito yomanga zipindayi ya Malawi Education Reform Program (MERP) yomwe cholinga chake ndi kufuna kuti ana a sukulu za pulayimale aziphunzila malo abwino kuti maphunziro ayende bwino ndipo igawidwa m’maboma osiyanasiyana mdziko muno.

Ntchitoyi ikuyembekezera kudzatha mu June chaka cha mawa ndi thandizo lochokera ku Banki yayikulu padziko lapansi.

Advertisement