Yemwe anali m’modzi mwa akulu akulu ku chipani cha Democratic Progressive DPP a Uladi Mussa ndipo pakali pano adalowa chipani cha Malawi Congress (MCP) ati iwo atafatsa kuwelenga malamulo a chipanichi tsopano ali ndi mangongolomela okapikisana nawo pa mipando iwiri ku msonkhano waukulu omwe chipani cha MCP chipangitse.
Poyankhula pa wailesi ya kanema wa Times ndi Brian Banda mu pulogalamu ya Times Exclusive, a Mussa ati iwo atawelenga malamulo a MCP akuona kuti malinga ndi luso lawo komanso nzeru zawo iwo akapikisana nawo pa mphando wa Wokopa anthu (Campaign Director) ngakhalenso pa mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri kumene.
A Mussa womwe atuluka ku ndende posachedwapa ati iwo ali ndi chikoka cha nkhani-nkhani kuti abweretse anthu kuchokera ku DPP popeza pano abweretsa kale ena ochuluka kubwera ku MCP.
“Ma udindo amewawa ndi amene ine ndikapikisane nawo ndipo ine ndiasapota a Chakwera mpaka 2030 wooh ndi imene ntchito imene agwire chenji golo imeneyo,” a Mussa anatero mkulongosola kwawo.
A Mussa MU mwezi wa Januwale analowa chipani cha MCP pa sukulu ya Pulayimale ya Katelera m’boma la Salima pamene chipani chawo chomwe anali Cha DPP chidawayimitsa kwa miyezi isanu ndi Inayi(9) chifukwa chophwanya dongosolo la chipanichi.
A Mussa womwe anali mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo cha pakati akhala akuthandiza a Kondwani Nankhumwa ndipo awiriwa adawachotsela limodzi pamodzi ndi ena omwe amayenda kuthandizila a Nankhumwa kuti adzayimile utsogoleri wa chipanichi ukadzafika msonkhano wawuku.