Mauthenga ena abodza akuika pa chiopsezo miyoyo ya anthu omwe ali ndi HIV — yatero NAC

Advertisement
hiv-ribbon

Bungwe la National Aids Commission (NAC) ladandaula ndi kukhudzidwa ndi mauthenga ochuluka komanso malonda okhudzana ndi machiritso a HIV ndi Edzi omwe akumafalitsidwa kwambiri.

Chikalata chomwe bungweli lalemba mosogozedwa ndi mkulu wake Betreace Lydia Matanje chati mauthenga komanso malonda abodza, osayenera komanso osokoneza ndioika pa chiopsezo miyoyo ya anthu ambiri omwe ali ndi HIV.

Chikalatachi chati anthu akuyenera kudziwa kuti m’dziko muno kulibe mankhwala ochiza HIV ndi Edzi ndipo chithandizo chomwe chilipo padakali pano ndi kumwa ma ARV omwe amagwira ntchito yoletsa kuchulukana kwa HIV m’magazi a anthu omwe anapezeka nayo.

Chikalatachi chawonjezera pofotokoza kuti mankhwala a ma ARV amachepetsa HIV m’thupi kufika pa mlingo oti siyingawonekenso ukayezetsa magazi ngati munthu wamwa mankhwalawa mwandondomeko koma sizitanthauza kuti HIV yatha m’thupimo .

“Vuto lilipo ndiloti zotsatira zimenezo zikumatanthauziridwa molakwikwa ndi anthu omwe akumanena kuti akuchiritsa HIV.”Iwo akumapereka zomwe amati ndi mankhwala ochiza HIV kapena kuwapempherera anthu omwe akumwa ma ARV ndipo amawalimbikitsa kuti apite kuchipatala kukatsimikiza kuti achira ku HIV. Anthu amakhulupirira zimenezi ndikusiya kumwa ma ARV, zotsatira zake HIV imayambanso kuchulukana m’thupi ndipo amafika podwala Edzi,” chatero chikalatachi.

Bungweli lati anthu akuyenera kudziwa kuti ndime 25 ya lamulo lothandizira kukhazikitsa ndondomeko za kapewedwe ndi ntchito zolimbana ndi mlili wa HIV ndi EDZI limaletsa kufalitsa mauthenga abodza, osayenera komanso osokoneza ntchito yolimbana ndi mlili wa HIV ndi EDZI.

NAC yati aliyense wochita motsutsana ndi lamuloli akupalamula mlandu ndipo akapezeka wolakwa ndi bwalo la milandu adzayenera kulipira chindapusa cha K5 miliyoni ndi kukhala kundende kwa zaka zisanu koma ngati ndi bungwe , lidzalipira chindapusa cha K10 miliyoni.

Bungweli latinso potsatira lamulo komanso mogwirizana ndi mabungwe ena monga a Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) ndi a Pharmacy Regulatory Authority (PMRA ) , adzatsata ndi kufufuza mauthenga onse abodza, osayenera komanso osokoneza ntchito yolimbana ndi mlili wa HIV ndi EDZI, ndipo wopezeka wolakwa adzaweruzidwa molingana ndi malamulo.

Advertisement