Ali mchitokosi kamba kochitira chiwembu wakabaza wa njinga yamoto

Advertisement

Apolisi ku Limbe mumzinda wa Blantyre akusunga mchitokosi bambo wina wa zaka 34 pamene iye ndi azake ena anayi anachitira chiwembu munthu wina woyendetsa njinga yamoto yakabaza ya mtundu wa Lifan LF 150-7 yomwe nambala yake ndi BT 12854 ndicholinga chofuna kumubera.

Nkhani yonse ikuti bamboyu yemwe dzina lake ndi Bright Maisa anagwilizana ndi mwini wake njingayo pa 11 February mwezi uno kuti amutenge akamusiye ku Chichiri kuchokera kwa Goliyo ku Ndirande.

Apa mwini njingayu adavomera kuti amutenga mkuluyu ndipo atafika ku Chichiriko pa malo ena padatulukira anzake a Maisa anayi omwe adayamba kumumenya wanjingayo uku akufuna kumukwangwanula njinga yake.

Ali mkati momumenya, mwamwayi kudatulukira galimoto ya polisi yomwe mkuti panthawiyi idali kupereka chitetezo munthawiyi ndipo apolisiwa adakwanitsa kugwira a Maisa pamene anzawo anayiwo adaliyatsa liwiro la mtondo odowoka.

Pakadali pano kafukufuku ali mkati ofufuza komwe anzawo a Maisa adathawira ndipo akapezeka akaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlanduwu

A Maisa amachokera m’mudzi wa Misanjo kwa mfumu yayikulu Chikumbu mboma la Mulanje.

Advertisement