Mary Navicha akana kuyankha za SONA mnyumba ya malamulo

Advertisement

Yemwe wangosankhidwa kumene kukhala mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) m’nyumba  yamalamulo, mayi Mary Navicha akana kulankhulapo m’nyumbayi pa zomwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera analankhula pomwe amatsekulira mkumano wa aphungu m’nyumbayi lachisanu.

Sipikala wanyumbayi a Catherine Gotani Hara anapeleka mwayi kwa a Navitcha womwe akudziwika m’nyumbayi ngati mtsogoleri wa DPP chabe koma a Navicha anangothokoza chifukwa chopatsidwa mpata oyankhula ndipo anati iwo anayankha kale zokhudza SONA kenako anakakhala pansi

A Navicha Lachiwiri anayankha za SONA panja pa nyumba ya malamulo  pomwe anatulutsidwa m’nyumbayi chifukwa chosokoneza poyendera lamulo 105 la mayendetsedwe a nyumbayi.

A sipikala Hara mwachidule auza a Navicha kuti zomwe alankhula kunja kwa nyumbayi sizinaikidwe ngati gawo lazokambirana m’nyumbayi chifukwa  zinali zosatsata ndondomeko komanso zoti sizinasungidwe ndi  zimtepamawu za m’nyumbayi.

Advertisement