Dziko la Malawi silikugwiritsa ntchito  kwambiri  makondomu

Advertisement

Dziko la Malawi pamodzi ndi mayiko ena onse padziko lapansi lachiwiri pa 13 Febuluwale limakumbukira nawo tsiku la “Condom” pamene akatswiri ati a Malawi ambiri sakutha kupeza mwayi wa makondomu mwachangu.

M’modzi mwa katswili owona za kulera ndi uchembele wabwino yemwenso ndi mkulu wa Family Planning and Association of Malawi (FPAM) Donald Makwakwa awuza wailesi ina kuti pakufunika kuti makondomu adzipezeka kwambiri kudzela mu njira zosiyanasiyana kuti kakhalidwe  kogwiritsa ntchito condom kazoloweledwe.

A Makwakwa anati nthawi zambiri m’malo momwe anthu amakapezamo makondomu amakapeza mulibe  pa nthawi yomwe iwo akufuna kugwiritsa ntchito zomwe zimakakamiza anthuwa kuti akapange mchitidwe ogonana mosadziteteza.

Achinyamata ena omwe talankhula nawo ati makondomu akuyenera kumapezeka kwambiri kuti achinyamata azolowere komanso adzisowa zifukwa zopangila mchitidwe ogonana mosadziteteza

Wachinyamata wina wa m’mudzi mwa Liti ku Zomba wati alangizi komanso amabungwe akabwera m’mamidzi akuyenera nthawi zonse kumakhala ndi ndondomeko yongogawa makondomu  mcholinga chofuna kuchepetsa matenda chifukwa zipatala mzotalikira.

A World Health Organization  (WHO) anaika tsiku lokumbukira kondomu ngati chida chodalilika chopewera matenda opatsilana pogonana komanso mimba zosakonzekera.

Zotsatila za kafukufuku yemwe anasindikizidwa pa 23 November okhudza kagwiritsidwe ntchito ka kondomu pakati pa achinyamata muno m’Malawi wawonetsa kut achinyamata ambiri sakugwiritsa ntchito kondomumokwanila  zomwe zagwirizana ndi  zotsatira za kafukufuku wina yemwe anachitika mu 2015/16  wa Malawi Demographic and healthy Survey,

Malinga ndi zotsatila za kafukufukuyu  amuna ambiri okwana 55 pa 100 aliwonse anagwiritsa ntchito kondomu mu miyezi inayi kafukufukuyu asanachitike kulekana ndi akazi amene anali 18 pa 100 aliwonse mu miyezi yomweyo.

Advertisement