“Ndani amapeza vuto ine ndikamwa mowa?” – wadabwa Namadingo

Advertisement
Namadingo said this in Times Exclusive interview with Brian Banda aired on Times Television on Saturday.

…wati u Doc wake pano ndiwa #DocAnavaya osati wa UNISA

Ngati munalibe bandulo ya intaneti kumathero a sabata yatha, zambiri zakuphonyani, komabe tikutsinani khutu pang’ono: Oyimba Patience Namadingo watsindika kuti iye siwoyimba nyimbo zauzimu, mukamuona alithapsa musadabwe, bibida amachita naye akatelo amakwera Mercedes Benz yake ndipo pamwamba pa zonsezo, akuti vuto lalikulu m’dziko muno ndi loti anthu ambiri ndiosaphunzira.

Loweruka usiku, pa 27 January, 2024, linali tsiku lina lomwe oyimba Namadingo anaphera mphongo kuti pena munthu umafikadi potopa ndipo ukatopa sumayang’anaso kuti pali apongozi koma umalavula zakukhosi zonse kuti wakumvayo amve osafunayo akhale.

Oyimbayu amacheza ndi mtolankhani Brian Banda mu pogalamu yapadera pa wayilesi ya Times ndipo zina mwa zinthu zomwe anakamba ndi monga kutsindika kuti iye siwoyimba nyimbo za uzimu koma wati ndi oyimba nyimbo zothandizira kusintha kaganizidwe ndi machitidwe azinthu pa anthu osiyanasiyana.

Apa Namadingo yemwe ndi mwini nyimbo yotchuka ya ‘Mtendere’, anati chidwi chake pano chinatsikira pa kuyimba nyimbo za chikondi potengera kuti bukhu lopatulika limalimbikitsa anthu kukhala owonetsa chikondi nthawi zonse komabe wati akafuna aziyimbaso nyimbo yauzimu ngakhale kuti wati padzikhala patalipatali.

“Nditha kudzizindikilitsa ngati “conscious kapena moral artist”. Ndimaimba zomwe ndikudziwa kuti zithandiza anthu. Ndine mkhilisitu , ngati nditafuna kuimba zokhudza Mulungu, ndiyimba ndipo ndayimbapo. Ndimaimbaso za chikondi. Chikondi ndi mutu waukulu mdziko lonse la pansi ndipo bukhu lopatulika limatilimbikitsa kugawa chikondi.

“Ndinayamba kuyimba nyimbo zauzimu koma panopa ndinagawa kuti ndizichita chikatikati. Zauzimu ndikuyimba, zinaso zomwe zikuchitika mdziko ndi kuyimba. Ngakhale tili akhilisitu oti tikupita ku mwamba, tikuyeneraso kudziwa kuti pa dziko tikukhalapa pali zinthu zomweso tikuyenera kuziunikira bwino,” watelo Namadingo.

Atafusidwa ngati zithuzi zomwe zikumazungulira m’masamba anchezo zomuonetsa iye ali thapsa kamba ka chakumwa chaukali zili zowona, oyimbayu, sanafune kuvala chikopa cha nkhosa ndipo wanenetsa kuti iye pokhala membala wa mpingo wa Katolika, bibida amachita nayedi ndipo akuti samaona vuto lili lonse kuti iye ndi chidakwa.

Apa Namadingo yemwe posachedwapa anapita ku tchuthi mdziko la America komwe akuti wakaphunzira zinthu zingapo zokhudza mayimbidwe, wati ana omwe amamusilira, asayambe kumwa mowa pano potsanzira iyeyu, koma wati anawo aphunzire kaye kenaka adzamwe mowa akadza maloza sukulu, ali ma khumutcha nthawi imeneyo.

“Inetu mowa ndimamwa ndipo sindikudziwa kuti kumwa kwanga kwa mowa ndi vuto la ndani limenelo. Akupeza mavuto ndi ndani chifukwa choti ine ndimamwa mowa? Ine ndi mkatolika nde musakambe zomwa mowa, zilibe vuto lili lonse. Anawo ngati akufuna kumwa mowa aphunzire kaye ndiye adzamwe mowawo ndikukawera mu Benz ngati yaineyo osati adzimwa pano asanakule. Inetu sindimwera mowa pakhomo pa makolo anga,” wateloso oyimbayu.

Oyimbayu anadodometsaso anthu ndi yankho yake pa nkhani yokhudza vuto lalikulu lomwe lakhudza dziko lino lomwe anati ndikusaphunzira kwa anthu ochuluka zomwe akuti zimabwezeletsa ntchito ya chitukuko mbuyo komaso wati anakakonda anthu anakahunzira monga zinakhalira ku Singapore.

“Choyambilira nchakuti mdziko muno tilibe anthu ophunzitsidwa bwino. Nde takhala tikukamba kuti utsogoleri woyipa, koma munaganizapo kuti zitha kuchitika kuti mtsogoleri wa bwino koma anthu akewo olakwika? Anthu okhala akukamba kuti momwe Kamuzu anamwalira zinakakhala bwino panakabwera Bingu Wa Mutharika kutanthauza kuti iye anali mtsogoleri wa bwino, koma funso nkumati kodi iyeyo ankatsogolera anthu abwino? Nde ndikaona dziko lathu, vuto lomwe ndinapeza ndi loti chiwerengero cha anthu osaphunzitsidwa bwino ndi chambiri,” watelo Namadingo.

Namadingo wanenetsaso kuti a Malawi asayembekezere kudzamuona akuyimba pa misonkhano ya ndale ponena kuti ngati angatelo, anthu ena adzakakamizika kuyamba kukonda anthu andale amenewo ngakhale atakhala kuti alibe mfundo zotukula dziko lino ndipo wati ngati andale otelowo angavoteledwe, zikutanthauza kuti naye wathandizira nawo kuti dziko lino liwonongeke.

Pa nkhani ya ulemu wa padera omwe sukulu yaukachenjede ya mdziko la South Africa inakana kuti siyinamupatse, Namadingo wati sukuluyi inapanga zimenezi kungofuna kumunyazitsa chabe ndipo wadabwa kuti sukuluyi ngati imanenedi chilungamo kuti siinapeleke ulemu umenewu, bwanji siyinamuthire dzingwe.

Apa namatetule pa mayimbidweyu wati anakakonda anakapatsidwa ulemu ndi sukulu yaukachenjede yakonkuno yomwe akuti siyikanapanga chipongwe cha mtunduwu koma wati sukulu ya kunjayi siyingaletse anthu omukonda kumutchula kuti dokotala ndipo wati pano samakhumudwa munthu akamuyitana kuti bambo (Mr) Namadingo.

“Sindimakhumudwa kundiyitana kuti Mr kapena Dr Namadingo, ndimayina chabe awa, anthu ondikonda amanditchulabe kuti Doc.

Advertisement