Pomwe masiku akusenderabe kuchitseko kuti dziko lino lichititse chisankho chaka cha mawa chino, chipani cha Democratic Progressive (DPP) chataya ena mwa mavoti ophaipha, kamba koti anthu ena otsatira a Kondwani Nankhumwa, ati nawoso atuluka nchipani ndipo dzuwa lili phwee, ang’amba nsalu za chipanichi.
Lamulungu pa 28 January, 2024, a Nankhumwa omwe posachedwapa pamodzi ndi anzawo ena angapo achotsedwa mu chipani cha DPP pa nkhani zokhudza kusasunga mwambo, anali ku dera la Ndirande munzinda wa Blantyre komwe anakhala nawo pa mwambo okhazikitsa m’busa Maxwell Ngwaya pa mpingo wa Makata CCAP.
Mwambowu utatha pomwe anayamba kubwelera ku nyumba kwawo, mkuluyu yemwe ku DPP anali otsatira kwa mtsogoleri mchigawo cha ku m’mwera, anawona ngati kutulo chinantindi cha anthu chitavumbuluka ndikumutchingira nsewu ndipo posakhalitsa kunayamba kuveka kuombedwa m’manja, kenaka nyimbo yomwe imati; “Nankhumwa, atiyankhule, Nankhumwa atiyankhule” inayamba kuimbidwa.
Mbali inayi amayi komaso achinyamata ena omwe anafika pa malowa atavala makaka a chipani cha DPP, anayamba kusonkhanitsa nsalu za chipanichi ndipo ena anayamba kuzing’amba nsaluzi uku akuyankhula mokwiya kwambiri amvekere; “ife timutsata Nankhumwa-yo. Apapa atichotsera limodzi”.
Malikhwelu anali fwiyo! Fwiyo! Mbali inayi nthungulu komaso nyimbo kuchokera kwa anthu omatsatilawo zikuimbidwa komaso ena uku akuvina nyimbo kuchokera pa chinkweza mawu chomwe chinali mgalimoto ya pa mdipiti wa mwana wa ku Mulanje-yu; a Nankhumwa sakanatha kudutsa pa malowa osatsukako mkamwa.
Polankhula kwa anthu omwe anamutchingira njirawa, Nankhumwa waulura kuti ngakhale wachotsedwa nchipani cha DPP, maloto ake onse anakali ndi moyo, ndipo wati chaka cha mawa apikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko komaso akuti sabata ino awuza mtundu wa a Malawi za tsogolo lake pa nkhani ya ndale.
“Chomwe andichotsera ndi chonena kuti ndimafuna ndikapikisane nawo ku konveshoni ya DPP kuti chaka cha mawa ndikapikisane nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko. Nde ndikutsimikizireni anthu akuno ku Malabada kuti maloto omwe ndinali nawo odzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko chaka cha mawa sanafe, anakalipo. Chaka cha mawa mundiona pa ballot paper,” wateloq Nankhumwa.
A Nankhumwa anapitilira ndikutsutsa mwantu wa galu mphekesera zomwe zakhala zikuveka posachedwapa kuti iwo ali ndi malingaliro ofuna kulowa chipani cha Malawi Congress (MCP) komaso United Transformation Movement (UTM).