Anyamata oshanganipa pa tauni anjatidwa ku Lilongwe


Anyamata oshanganipa pa tauni anjatidwa ku Lilongwe

Makosana awili ku Lilongwe athilidwa zingwe ndi apolisi kamba kowaganizira kuti akhala akubera anthu ponamizira kuti ndi ochita bizimezi yoyendetsa galimoto zonyamula anthu.

Nkhani yonse ikuti makosana awiliwa omwe mayina awo ndi a Alick Kazembe azaka 42 zakubadwa komanso a Moses Mponda azaka 35, lamulungu lapitali adanyamula bambo wina pa Roundabout ya MRA nthawi mkuti ili cham’ma 8 koloko usiku.

Munthawiyi makosanawa adali kugwilitsa ntchito galimoto la mtundu wa Swift yomwe nambala yake ndi LA 8878.

Atafika pa Estate ya Balon, njonda ziwilizi zidakwangwanula bamboyo katundu osiyanasiyana wandalama zokwana k700, 000.

Apolisi ya Lilongwe atatsinidwa khutu za chipongwechi adachita kafukufuku adapeza wina mwa katundu obedwayu ndi kukhwidzinga anyamata awili okhudzidwa pa chipongwechi ndipo pakadali pano akusakanso anthu ena omwe akuwaganizira kuti adalinso limodzi.

Pakadali pano Makosanawa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu komwe akayankhe mlandu wakuba

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.