Boma la Mwanza lakwanitsa kuthesa ma ukwati a ana okwana 118

Advertisement
Mwanza council hosted their counterparts from Zomba District Council on an 'Ending Child Marriages' learning visit supported by Save the Children.

Mkulu wa Mwanza Social Welfare, a Mary Msidwa, ati boma la Mwanza lakwanitsa kuthetsa maukwati a ana achichepere okwana 118 mu chaka cha 2023.

A Msindwa anena izizi lero pamene anali ndi zokambilana  ndi khosolo la boma la Zomba komaso bungwe la Save the Children pa mutu oti “Kuthetsa maukwati a ana achichepere”.

Iwo ati bhodi yawo yakonza misonkhano yosiyanasiyana yomwe ithandizire kuchepetsa mchitidwe okwatitsa ana achichepere m’bomali.

Mr Christopher Ndaona omwe ndi mkulu wa Zomba Social Welfare ati mkumanowu wathandizira kuwatsekula  maso m’mene angagwirire ntchito yothetsa ma ukwati a ana achichepere.

Boma la Zomba linapeza ma ukwati a ana achichepere okwana 645 mu chaka cha 2023.

Mkulu oyang’anira ntchito za chuma komaso zitukuko Ku bungwe la Save the Children a McPherson Kapalamula ati bungwe lawo lipitiliza ntchito yothandiza ma khosolo amaboma awiriwa ndi cholinga choti mchitidwe uwu utheretu.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement